Mzimu wa dziko ndi kaganizidwe ka anthu kosadalira Nzeru za Mulungu koma kotsogoleledwa ndi Satana (Aefeso 2:2; 1 Akorinto 2:12)
Timadziwa kuti kuli mpweya (mphepo) tikaona m'mene imagwirira ntchito. Ndi m'menenso mpweyawu (kaganizidwe kameneka) kalili; timadziwa kuti ulipo tikaona ntchito zake popeza umadalira kaganizidwe ka anthu ndi Satana.
Tiyenera kumalemekeza ulamuliro m'banja, mu mpingo ndi maulamuliro a m'dziko kuti zinthu zizichitika mwadongosolo ndi mwa mtendere. -Aroma 13:1, 2. Tiyenera kumamvera maulamuliro a m'dziko popedza palibe olamulira yemwe amakhalapo popanda kuloledwa ndi Mulungu. Koma ngati atilamula kuchita zinthu zotsutsana ndi mfundo za m'Mawu a Mulungu, tiyenera kumvera Mulungu kuposa anthu. (Machitidwe 5:29) Tiyenera kuchita zimenezi popeza sitili mbali ya dziko. -Yohane 17:16
Tiyenera nthawi zonse kuyetsetsa kukhala ndi makhalidwe omwe Mzimu wa Yehova umasonyeza.
Tiyeneranso kupewa ntchito za thupi. (Agal. 5:19-21) Ngati tingamwe mwauchidakwa Yehova adzatiimbabe mlandu ngakhale tili kwatokha (kapena kunyumba kwathu).
Kuti tidzapeze moyo wosatha tiyenera kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Anthu ena amalephera kulimbitsa ubwenzi wawo chifukwa amakhala otanganidwa ndi ntchito kuti apeze zipangizo zamakono kapena kupita ku dziko lina kuti akafunefune chuma kapenanso kukala ndi ntchito yowonjezera nkumalephera kusonkhana.-1 Yohane 2:.15-17
Tiyenera kuyetsetsa kumakhala ndi moyo wosalira zambiri kuti tipitirize kuchita utumiki wathu nkumakondweretsa Yehova chifukwa ubwenzi wathu ndi Yehova ndi omwe udzatithandize kuti tidzapeze moyo wosatha osati chuma (Mateyu 5:8)