7 Kodi Yeremiya anakumana ndi mavuto ati ndipo kodi nthawi zina ankamva bwanji?
7 Abale athu ambiri amatumikira m’madera amene amafunika kupirira kwambiri. Mneneri Yeremiya anatumikiranso m’dera lotereli. Iye ankalalikira mu ufumu wa Yuda utatsala pang’ono kuwonongedwa ndipo iyi inali nthawi yovuta kwambiri. Tsiku lililonse chikhulupiriro cha Yeremiya chinkayesedwa chifukwa chomvera Mulungu pogwira ntchito yolalikira uthenga wa chiweruzo Chake. Pa nthawi ina ngakhale Baruki, yemwe anali mlembi wake wokhulupirika, anadandaula chifukwa chotopa.
8 Malinga ndi
8 Koma Yeremiya sanasiye ntchito yake. Iye anapitiriza kudalira Yehova. Zotsatira zake zinali zakuti mneneriyu anaona kukwaniritsidwa kwa mawu a Yehova olembedwa pa
9 Mofanana ndi mtengo wa zipatso wobiriwira “wobzalidwa m’mphepete mwa madzi” kapena m’munda wa zipatso wothiriridwa bwino, Yeremiya ‘sanasiye kubala zipatso.’ Iye sanalole kufooketsedwa ndi anthu oipa amene ankamunyoza. M’malomwake, iye nthawi zonse ankadalira Kasupe wa “madzi” opatsa moyo ndipo ankatsatira zonse zimene Yehova anamuuza.
10 Kodi tili ndi madalitso otanindipo tiyenera kudzifunsa funsoliti?
10 Yehova watipatsa paradaiso wauzimu wokhala ndi zinthu zambiri pofuna kutithandiza kuti tipirire mavuto a pa moyo wathu masiku otsiriza ano. Zina mwa zinthu zimene watipatsa ndi Baibulo lonse, lomwe ndi Mawu ake, ndipo likumasuliridwa molondola m’zinenero zambirimbiri. Iye wapereka chakudya chauzimu chambiri ndiponso pa nthawi yake kudzera mwa gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Iye watipatsanso abale ndi alongo amene amatilimbikitsa tikamacheza nawo pa misonkhano yampingo ndi ikuluikulu. Kodi mumagwiritsa ntchito mokwanira zinthu zimene watipatsazi? Anthu onse amene amagwiritsa ntchito mokwanira zinthu zimenezi “adzafuula mokondwa chifukwa chokhala ndi chimwemwe mumtima.” Koma amene samvera Mulungu ‘ adzalira chifukwa chopwetekedwa mtima ndipo adzafuula chifukwa chosweka mtima.’