Tiyerekezere kuti anthu ali akuoloka nyanja ndipo ali m'boti. Koma atangosala ndi mamita 15 kuti afike pamtunda, boti likuchita ngozi ndipo anthu akusambira kuti apulumutse miyoyo. Kodi chingachitike nchiyani ngati pambuyo pongosambira kwa mamita 10 munthu wina wasiya kusambira chifukwa chotopa? Angamire. Choncho ifenso tikuyenera kupilira mpaka mapeto, monga momwe Yesu ananenera pa maliko 13:13.
Naomi ankafunika kupilira chifukwa mwamuna wake ndi ana ake awiri atamwalira motsatizana. Koma Yehova anamudalitsa chifukwa anamudalira ndipo anapilira.
Anthufe tinabadwa ndi mzimu (mtima) ofuna kukondedwa, choncho zimakhala zovuta kupilira ngati ena ayamba kutida. Zikatero chikhulupiliro cha munthu chimatha kutekeseka. Ngakhalenso Yesu anakumana ndi chiyeso chimenechi koma iye anachigonjetsa. Abale ake ndi anthu ena ankumunyoza nkumati wapenga kapena amatulutsa ziwanda pogwiritsa ntchito mphamvu ya wolamulira ziwanda. Iye ankaganizira madalitso omwe adzapatsidwe mtsogolo, nchifukwa chake anapilirabe. (Aheber 12:2-4)
Ngati m'bale kapena mlongo sakupedza munthu woyenera kukwatirara naye (2 Akorinto 6:14-18) angayambe kuganiza kuti bola angotenga munthu aliyense ngakhalenso oti si mboni. Koma timayenera kukumbukira kuti Yehova sanasinthe m'mene amaionera nkhaniyi. --(1 Mafumu 11:4; 1 Akorinto 7:39)
Pamene ankakwanitsa zaka 84, mneneri wamkazi Anna anakhala ndi mwamuna wake kwa zaka 7 zokha kuchokera pa unamwali wake. Iye anapilira kwa zaka zonse zomwe sanali pa banjazi chifukwa nthawi zonse ankatanganidwa ndi kuchita zinthu zokhunza kulambira. (Luka 2:36, 37)
Ifenso tiyenera kumayetsetsa nthawi zonse kuika patsogolo zofuna za Yehova (Mateyu 6:33) ndipo tisakhale ngati akhristu a ku Efeso omwe anasiya kukonda Yehova patapita nthawi. (Chivumbulutso 2:1-5)