Chikondi ndi chinthu chomwe chingapangitse anthu kukhala mabwenzi. Timapedza madalitso monga Chmwemwe poti Yehova ndiye anatikoka. -1 Tim. 1:11
Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse ndipo ilo ndi m'bale amene anabadwa kuti akuthandize ukagwa m'mavuto. -Miy. 17:17; 27:9
Ubwenzi weniweni umakhala opanda mpeni ku mphasa. Banja lomwe anthu ake anakwatirana chifukwa chokondana, silimatha. -1 Akorinto 13:8.
Rute anali ndi chikondi chenicheni (kwa mpongozi wake Naoni) ndipo analolera kusiyana ndi achibale ake ngakhalenso milungu yake kuti azikakhala naye. Ifenso tiyenera kutsanzira chikondi chenicheni ngati chimenechi.
Anthuwa anali pa ubwenzi wabwino ngakhale kuti anali a misinkhu yosiyana (ankasiyana ndi zaka pafupifupi 30.) Ankasonyezana chikondi chenicheni chifukwa choti onse ankakondana komanso kulemekezana. - Aheb. 13:7
Yesu analolera kufera ophunzira ake powasonyeza chikondi, ndipo ifenso tidzikhala okonzeka kufera ena ngati pangafunike kutero.
Abrahamu anali okonzeka kupha mwana wake chifukwa ankadziwa kuti Yehova adzamuukitsa. (Aheb. 11:6)